Isaac Jomo Osman, amenenso amatchuka kuti Ntopwa 1 ndi membala wa Democratic Progressive Party (DPP) komanso Councillor wa Bangwe Mthandizi Ward. Ngakhale adakulira kwa Ntopwa, adabadwila ku Zambia, komwe adachokako adakali mwana kupita ku Mangochi. Atangoyamba kumene chinyamata adachokako nkupita ku Limbe komwe adayamba maganyu, kunenelela ma minibus mpaka kufika popeza mgodi (Chairman oyang'anira achinyamata onenela ma minibus ku Limbe). Adalowa ndale ngati membala wa DPP, kuimila ngati khansala. Adayambitsanso ma team ampira a Ntopwa Football Club komanso Ntopwa Netball Club. Pano zinthu zikuoneka kuti zidavuta chifukwa wamangidwapo kangapo konse chifukwa cha zimene adachita maka pamene DPP inkalamula. Jomo ndi munthu amenenso amatchuka ndi zochita zachisawawa komanso zipolowe. Panthawi ina adaoneka akuzunza membala wa MCP pamene munthuyo adavala malaya amakaka aMCP mumsika wa Limbe.
Ещё видео!